CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzifunsira Nzeru kwa Yehova
Aisiraeli anapempha malangizo kwa Yehova mobwerezabwereza (Owe 20:17, 18, 23; w11 9/15 32 ¶2)
Yehova ankawayesa Aisiraeli kuti aone ngati anali ofunitsitsa kuchotsa zinthu zoipa (Owe 20:26-28; w05 1/15 27 ¶8)
Tiyenera kupitiriza kufufuza malangizo a Yehova tikamakumana ndi mavuto (Owe 20:35; Lu 11:9; w11 9/15 32 ¶4)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Ndikakumana ndi mayesero, kodi nthawi yomweyo ndimapempha Yehova kuti andithandize? Kodi nthawi zonse ndimadalira Yehova kuti andipatse nzeru komanso anditsogolere?’