CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Yehova Angakuthandizeni Kuti Mukwanitse Kuchita Utumiki Wovuta
Alevi omwe anali alonda apachipata anali ndi udindo waukulu kwambiri (1Mb 9:26, 27; w05-CN 10/1 9:8)
Pinihasi anali mtsogoleri wa alonda a pachihema m’nthawi ya Mose (1Mb 9:17-20a)
Yehova anathandiza Pinihasi kukwaniritsa utumiki wake (1Mb 9:20b; w11-CN 9/15 32:7)
Yehova amatipatsa zochita zambiri zomwe zimakhala zofunika. Ngati simukudziwa bwino mmene mungachitire utumiki winawake, muzipemphera kwa Yehova komanso muzipempha Mkhristu wodziwa zambiri kuti akuthandizeni.—Afi 2:13.