Chithunzi chapachikuto: Davide akupereka anthu ogwira ntchito komanso zipangizo zomangira kachisi kwa Solomo
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzithandiza Achinyamata Kuti Azichita Zambiri
Davide ankadziwa kuti mothandizidwa ndi Yehova, Solomo adzakwanitsa kuyang’anira ntchito yonse yomanga kachisi (1Mb 22:5; w17.01 4:8)
Davide analimbikitsa Solomo kuti azidalira Yehova n’kumachita zoyenera (1Mb 22:11-13)
Davide anali wofunitsitsa kuthandiza Solomo (1Mb 22:14-16; w17.01 4:7; onani chithunzi chapachikuto)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingathandize bwanji achinyamata amumpingo mwathu kuti azisangalala komanso azichita zambiri potumikira Yehova?’—w18.03 11-12:14-15.