CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzikhalabe Wosangalala Ngakhale Pamene Zinthu Sizikuyenda Bwino
Davide ankafunitsitsa kumangira Yehova kachisi wokongola (1Mb 17:1, 2; w06-CN 7/15 19:1)
Yehova anauza Davide kuti iye si amene adzamange kachisiyo (1Mb 17:4)
Davide sanafooke koma anapitirizabe kugwira ntchito imene Yehova anam’patsa (1Mb 17:7; 18:14)
Ngati simungakwanitse kuchita utumiki winawake chifukwa cha msinkhu, thanzi kapena zinthu zina, musamafooke koma muzingochita zimene mungakwanitse kuchitazo.—Mac 18:5; w21.08 33:11.