CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzithandiza Ena Kuti Azichita Zambiri
Moredekai anapereka chitsanzo chabwino cha kukhala wolimba mtima komanso wokhulupirika kwa Yehova (Est 3:2-4; it-2 431:7)
Anathandiza Esitere kuona kuti akhoza kuchita zabwino (Est 4:7, 8; it-2 431:9)
Analimbikitsa Esitere kuti akhale wolimba mtima komanso azidalira Yehova (Est 4:12-14; ia 16:22-23)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zolankhula komanso zochita zanga zimathandiza ena mumpingo kuti azichita zambiri potumikira Yehova?’