MBIRI YA MOYO WANGA
Mlangizi Wamkulu Wakhala Akutiphunzitsa Kwa Moyo Wathu Wonse
PA UTUMIKI wathu wa upainiya komanso umishonale, ine ndi mkazi wanga takhala tikukumana ndi zoopsa monga malodibuloko okhala ndi asilikali a mfuti, zinthu zitayatsidwa mumsewu, mvula kapena mphepo yamkuntho komanso kuthawa m’nyumba zathu. Ngakhale kuti tinkakumana ndi mavuto onsewa, tinkakhalabe osangalala chifukwa cha zimene tinasankha. Pa moyo wathu wonse taona Yehova akutithandiza komanso kutidalitsa. Mlangizi Wamkulu Yehova wakhala akutiphunzitsa zinthu zofunika.—Yobu 36:22; Yes. 30:20.
CHITSANZO CHA MAKOLO ANGA
Chakumapeto kwa chaka cha 1950, Makolo anga anasamuka kuchoka ku Italy kupita kutauni ya Kindersley m’chigawo cha Saskatchewan ku Canada. Pasanapite nthawi yaitali, iwo anaphunzira choonadi ndipo chinakhala chofunika kwambiri pa moyo wathu. Ndimakumbukira kuti ndili mwana, nthawi zambiri ndinkakhala mu utumiki ndi anthu a m’banja langa, choncho ndimakonda kunena moseka kuti ndinayamba upainiya wothandiza ndili ndi zaka 8.
Banja lathu cha m’ma 1966
Makolo anga anali osauka komabe ankapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yodzimana kuti azitumikira Yehova. Mwachitsanzo, mu 1963, iwo anagulitsa katundu wawo wambiri kuti apeze ndalama n’cholinga choti akapezeke kumsonkhano wa mayiko womwe unachitikira ku Pasadena ku California m’dziko la U.S.A. Mu 1972 tinasamukira mumzinda wa Trail ku British Columbia m’dzilo la Canada, womwe unali mtunda wa makilomita 1,000, kuti tikathandize m’gawo lolankhula Chitaliyana. Bambo anga ankakana kukwezedwa pa ntchito n’cholinga choti aziika maganizo awo onse pa kutumikira Yehova.
Ndimayamikira kwambiri chitsanzo chimene makolo anga anatipatsa ineyo ndi azibale anga atatu. Zimene anatiphunzitsa ndi zosaiwalika ndipo zandithandiza pa utumiki wanga wonse. Ndaphunzira kuti ndikamaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, Yehova adzandisamalira.—Mat. 6:33.
KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
Mu 1980, ndinakwatira mlongo wina wokongola dzina lake Debbie, yemwe anali ndi zolinga zotumikira Yehova. Tinkafuna kuchita utumiki wa nthawi zonse. Choncho Debbie anayamba upainiya patangopita miyezi itatu kuchokera pamene tinakwatirana. Patatha chaka chimodzi, tinasamukira mumpingo wina waung’ono komwe kunkafunika olalikira Ufumu ambiri, ndipo inenso ndinayamba kuchita upainiya.
Pa tsiku la ukwati wathu mu 1980
Patapita nthawi tinakhumudwa ndipo tinaganiza zoti tichokeko. Koma choyamba tinalankhula ndi woyang’anira dera. Iye anatiyankha mwachikondi koma moona mtima kuti: “Mbali inatu vuto ndi inuyo. Mukungoganizira zimene sizikuyenda bwino. Ngati mutati mufufuze zimene zikuyenda bwino mukhoza kuzipeza.” Apatu anatipatsa malangizo amene timafunikira. (Sal. 141:5) Nthawi yomweyo tinayamba kuwatsatira ndipo tinazindikira kuti panalidi zabwino zambiri zimene zinkachitika. Anthu ambiri mumpingo anayamba kufuna kuchita zambiri potumikira Yehova, kuphatikizapo achinyamata ndi ena omwe anali pabanja ndi osakhulupirira. Apa tinaphunzirapo zambiri. Tinaphunzira kuti tiziganizira zimene zikuyenda bwino kwinaku tikuyembekeza kuti Yehova akonze zimene sizikuyenda bwino. (Mika 7:7) Tinayambiranso kusangalala ndipo zinthu zinasintha.
Alangizi a sukulu yathu ya upainiya anali atatumikirapo m’mayiko ena. Iwo anationetsa zithunzi zosonyeza mavuto ndi madalitso amene anapeza. Izi zinatilimbikitsa kuti tiyambe kufuna kuchita umishonale, moti tinatsimikiza kuti tiyambe utumiki umenewu.
Tili pa Nyumba ya Ufumu, ku British Columbia mu 1983
Kuti tikwaniritse cholinga chathuchi, mu 1984 tinasamukira kugawo lolankhula Chifulenchi m’dziko la Quebec, womwe ndi mtunda woposa makilomita 4,000 kuchokera ku British Columbia. Tinkafunika kuphunzira chikhalidwe ndi chilankhulo chatsopano. Pa nthawi ina tinkangodalira kukatolatola mbatata zotsala m’munda wa mlimi wina. Debbie ankapeza njira zosiyanasiyana zophikira mbatatazo. Ngakhale kuti tinkakumana ndi mavuto, tinkapirira mosangalala ndipo tinkaona kuti Yehova akutisamalira.—Sal. 64:10.
Tsiku lina tinalandira foni yomwe sitinkayiyembekezera. Inali yotiitana kuti tizikatumikira ku Beteli ya ku Canada. Sitinkadziwa chochita chifukwa tinali titalemba fomu yofunsira Sukulu ya Giliyadi. Komabe tinavomera n’kupita. Titafika tinafunsa M’bale Kenneth Little wa m’Komiti ya Nthambi kuti, “Nanga za Sukulu ya Giliyadi tinafunsira zija?” Iye anatiyankha kuti, “Musadye mfulumira, ingodikirani.”
Patangopita mlungu umodzi, tinamvetsa zimene m’bale uja ankatanthauza. Ine ndi Debbie tinaitanidwa kuti tikalowe Sukulu ya Giliyadi. Choncho tinkafunika kusankha chochita. M’bale Little anatiuza kuti: “Dziwani kuti kaya musankha zotani, tsiku lina muzidzaonabe kuti bola mukanasankha zinazo. Palibe choposa chinzake. Yehova akhoza kudalitsa chilichonse.” Tinavomera kupita ku Giliyadi ndipo kwa zaka zambiri, taona kuti zimene M’bale Little ananena ndi zoona. Ifenso takhala tikupereka malangizo omwewa kwa anthu amene akufuna kusankha utumiki woti achite.
TINAYAMBA UMISHONALE
(Kumanzere) Ulysses Glass
(Kumanja) Jack Redford
Tinasangalala kukhala m’gulu la ophunzira 24 amene analowa kalasi ya nambala 83 ya Sukulu ya Giliyadi. Tinakalowa sukuluyi ku Brooklyn mumzinda wa New York, mu April 1987. Alangizi athu anali M’bale Ulysses Glass ndi M’bale Jack Redford. Miyezi 5 inatha msanga ndipo tinamaliza maphunziro athu pa 6 September, 1987. Tinatumizidwa ku Haiti limodzi ndi banja la John ndi Marie Goode.
Tili ku Haiti mu 1988
Kungoyambira mu 1962, pamene amishonale anathamangitsidwa, ku Haiti kunali kusanapitenso amishonale ena. Patangopita milungu itatu kuchokera pamene tinamaliza maphunziro a Giliyadi, tinkatumikira mumpingo wina wa ofalitsa 35, womwe unali m’dera lamapiri. Tinali achinyamata ndipo sitinkadziwa zambiri. Tinkakhalanso tokhatokha m’nyumba ya amishonale. Anthu ambiri kumeneko anali osauka ndipo sankatha kuwerenga. M’masiku oyambirira a umishonale wathu kunali zipolowe, kuukira boma, kuotcha zinthu m’misewu komanso mphepo ndi mvula zamkuntho.
Tinaphunzira zambiri kwa abale ndi alongo a ku Haiti omwe ankakhalabe osangalala ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Ambiri ankavutika komabe ankakonda Yehova komanso utumiki. Mlongo wina wachikulire sankatha kuwerenga koma analoweza mavesi pafupifupi 150. Vuto lililonse lomwe tinkakumana nalo linkatilimbikitsa kuti tizilalikira uthenga wabwino womwe udzathetse mavuto a anthu. Timasangalala kuona kuti anthu ambiri amene tinkaphunzira nawo Baibulo anadzakhala apainiya okhazikika, apainiya apadera komanso akulu.
Tili ku Haiti, tinakumana ndi Travor yemwe anali mmishonale wa chipembedzo cha Chimomoni ndipo tinakambirana zokhudza Baibulo maulendo angapo. Patapita zaka zingapo ndinalandira kalata yake. Analemba kuti: “Ndibatizidwa pamsonkhano wadera ukubwerawu, ndikufuna kuti ndibwerere ku Haiti ndikakhale mpainiya wapadera m’dera limene ndinkalalikiramo ngati mmishonale wa Chimomoni lija.” Iye anachitadi zimenezo ndi mkazi wake kwa zaka zambiri.
TINAPITA KU EUROPE KENAKO KU AFRICA
Tikutumikira ku Slovenia mu 1994
Tinatumizidwa ku Europe komwe ntchito yolalikira inali itayamba kukula. Mu 1992 tinafika ku Ljubljana m’dziko la Slovenia, dera la kufupi ndi kumene makolo anga anakulira asanasamukire ku Italy. Nkhondo inali ikupitirirabe m’madera a dziko limene linkatchedwa Yugoslavia. Nthambi ya ku Vienna ku Austria komanso maofesi a ku Zagreb, Croatia, Belgrade ndi Serbia ndi amene ankayang’anira ntchito yolalikira m’maderawa. Tsopano dera lililonse lomwe linalandira ufulu wokhala dziko palokha linkafunika kukhalanso ndi Beteli.
Apa tinafunikanso kuphunzira chikhalidwe ndi chilankhulo china. Anthu a kuderali ankakonda kunena kuti, “Jezik je težek,” kutanthauza kuti “Chilankhulo chathu ndi chovuta” ndipo chinali chovutadi. Abale ndi alongo kumeneko anali okhulupirika ndipo ankatsatira malangizo alionse amene gulu lathu lapereka. Tinkachita nawo chidwi kwambiri ndipo tinaona mmene Yehova anawadalitsira. Tinaonanso mmene Yehova amakonzera zinthu pa nthawi yoyenera. Pa zaka zimene tinakhala ku Slovenia, tinaona ubwino wa zimene tinaphunzira komanso tinaphunzira zinthu zambiri zatsopano.
Koma tinakumana ndi mavuto enanso. Mu 2000, tinatumizidwa ku Côte d’Ivoire, ku West Africa. Ndiyeno mu November 2002 kunali nkhondo ndipo tinauzidwa kuti tisamukire ku Sierra Leone. Kumeneko nkhondo yomwe inali itatenga zaka 11 inali itangotha kumene. Zinali zovuta kusamuka mwadzidzidzi ku Côte d’Ivoire. Koma mfundo zimene tinaphunzira zinatithandiza kukhalabe osangalala.
Tinkaganizira za anthu ambiri omwe ankafuna kuphunzira Baibulo komanso abale ndi alongo ambiri achikondi omwe anali atapirira nkhondo kwa zaka zambiri. Iwo anali osauka koma anali okonzeka kugawana ndi ena zimene anali nazo. Mlongo wina anam’patsa mkazi wanga zovala. Mkazi wanga akukayikira zoti alandire mlongoyo anamuuza kuti: “Pa nthawi ya nkhondo abale ndi alongo a m’mayiko ena ankatithandiza. Tsopano ndi nthawi yathu yoti tikuthandizeni.” Tinali ofunitsitsa kutengera chitsanzo chawo.
Tinabwerera ku Côte d’Ivoire koma zachiwawa zinayambiranso. Mu November 2004, tinasamutsidwa pa helokopita ndipo aliyense ankaloledwa kunyamula chikwama cholemera 10kg basi. Usiku umenewo tinakagona kukampu ya asilikali a ku France ndipo tinagona pansi penipeni. Tsiku lotsatira tinakwera ndege yopita ku Switzerland. Tinafika kunthambi cha pakati pa usiku ndipo abale a m’Komiti ya Nthambi komanso alangizi a Sukulu Yophunzitsa Utumiki limodzi ndi akazi awo anatilandira bwino. Iwo anatihaga, kutipatsa chakudya chotentha komanso machokoleti a m’dzikolo. Zimenezi zinatithandiza kuona kuti amatikonda kwambiri.
Mu 2005 ku Côte d’Ivoire, ndikulankhulana ndi abale othawa kwawo
Tinatumizidwa ku Ghana kwa kanthawi kochepa ndipo kenako nkhondo itacheperako tinabwereranso ku Côte d’Ivoire. Kukoma mtima kwa abale ndi alongo kunatithandiza pa nthawi yovuta yomwe tinkasamukasamukayi komanso pamene utumiki wathu unkasinthasintha. Ngakhale kuti abale ndi alongo amasonyezana chikondi mkati mwa gulu la Yehova, ine ndi Debbie tinagwirizana kuti tisamaone mopepuka zimenezi. Pambuyo pake tinazindikira kuti pa nthawi yovutayi tinaphunzira zinthu zambiri.
TINATUMIZIDWA KU MIDDLE EAST
Tili ku Middle East mu 2007
Mu 2006, tinalandira kalata kuchokera ku likulu lathu yotidziwitsa kuti tizikatumikira ku Middle East. Apanso tinkayembekezera kuphunzira zilankhulo ndi zikhalidwe zatsopano komanso kukumana ndi mavuto atsopano. Panali zambiri zoti tiphunzire m’derali lomwe munali mavuto chifukwa cha ndale komanso zipembedzo. Tinkakonda kwambiri zilankhulo zomwe zinkalankhulidwa m’mipingo yosiyanasiyana ndipo tinkaona kuti kutsatira malangizo amene gulu limatipatsa kumachititsa kuti tikhale ogwirizana. Tinkayamikira kwambiri abale ndi alongo omwe molimba mtima ankapirira kutsutsidwa ndi achibale awo, anzawo a kusukulu, a kuntchito komanso oyandikana nawo nyumba.
Tinapezeka nawo pamsonkhano wapadera womwe unachitika mu 2012 ku Tel Aviv m’dziko la Israel. Kuchokera pa Pentekosite wa mu 33 C.E., umenewu unali msonkhano woyamba womwe anthu a Yehova anasonkhana ochuluka choncho. Imeneyitu inali nthawi yosaiwalika.
Tinkapita kukayendera abale m’dziko limene ntchito yathu inali yoletsedwa. Tinkatenga mabuku athu, kulalikira komanso kuchita nawo misonkhano yomwe pankakhala anthu ochepa. Asilikali onyamula zida komanso malodibuloko zinali paliponse. Komabe tinkadzimva kukhala otetezeka tikamayenda mosamala ndi abale ochepa.
KUBWERERA KU AFRICA
Ndikukonzekera nkhani ku Congo mu 2014
Mu 2013, utumiki wathu unasintha ndipo tinatumizidwa kukatumikira ku nthambi ya ku Kinshasa m’dziko la Congo. Dzikoli ndi lalikulu komanso lokongola koma ndi losauka kwambiri ndiponso kumachitikachitika nkhondo. Poyamba tinkadziuza kuti, “Ku Africa timadziwako ndipo ndife okonzeka kupita.” Koma panali zambiri zoti tiphunzire makamaka pa nkhani yoyenda m’madera omwe kunalibe zinthu zambiri kapenanso misewu. Tinkaganizira zinthu zambiri zabwino zimene zinkachitika. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ankapirira komanso kukhalabe osangalala ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto a zachuma. Iwo ankakonda ntchito yolalikira komanso ankachita khama kupezeka pamisonkhano ikuluikulu komanso yampingo. Tinaona mmene ntchito ya Ufumu inkapitira patsogolo chifukwa chakuti Yehova ankatidalitsa komanso kutithandiza. Tinaphunzira zambiri pa utumiki wathu ku Congo ndipo tinapeza anzathu ambiri.
Tikulalikira ku South Africa mu 2023
Chakumapeto kwa 2017, tinapemphedwa kuti tipite ku South Africa. Tinali tisanatumikirepo kunthambi yaikulu ngati imeneyi ndipo mautumiki amene tinapatsidwa analinso atsopano. Panalinso zambiri zoti tiphunzire koma zimene tinaphunzira m’mbuyomo zinatithandiza. Timayamikira kwambiri abale ndi alongo amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Ndipo n’zochititsa chidwi kuona anthu a m’banja la Beteli akuchita zinthu mogwirizana kwambiri ngakhale kuti ndi osiyana mitundu ndi zikhalidwe. N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa anthu ake powapatsa mtendere chifukwa chakuti akuyesetsa kuvala umunthu watsopano komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo.
Pa zaka zimenezi, ine ndi Debbie takhala tikulandira mautumiki osangalatsa komanso kuphunzira zilankhulo ndi zikhalidwe zatsopano. Si nthawi zonse pamene zinali zophweka koma Yehova wakhala akutisonyeza chikondi chokhulupirika kudzera mwa abale ndi alongo komanso gulu lake. (Sal. 144:2) Timaona kuti zimene taphunzira pa utumiki wa nthawi zonse zatithandiza kuti tikhale atumiki abwino a Yehova.
Ndimayamikira kwambiri makolo anga chifukwa cha zimene anandiphunzitsa. Ndimayamikiranso mkazi wanga Debbie yemwe wakhala akundithandiza komanso chitsanzo chabwino cha abale ndi alongo padziko lonse. Tikamaganizira za moyo wathu wa m’tsogolo, ine ndi mkazi wanga Debbie, ndife otsimikiza kuti tipitiriza kuphunzitsidwa ndi Mlangizi Wamkulu Yehova.