Lachiwiri, July 15
Weta ana a nkhosa anga.—Yoh. 21:16.
Mtumwi Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (1 Pet. 5:1-4) Ngati ndinu mkulu, timadziwa kuti mumakonda abale ndi alongo anu ndipo mumafuna kuwasamalira. Komabe, nthawi zina mungamaone kuti mwatanganidwa kapena mwatopa kwambiri moti simungathe kukwaniritsa udindowu. Zikatere, kodi mungatani? Muzimuuza Yehova nkhawa zanu zonse. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikira ena, aziwatumikira modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Pet. 4:11) Abale ndi alongo anu angakumane ndi mavuto omwe sangatheretu panopa. Koma muzikumbukira kuti “m’busa wamkulu,” yemwe ndi Yesu Khristu, angawathandize kuposa wina aliyense. Iye angawathandize panopa komanso m’dziko latsopano. Mulungu amangofuna kuti akulu azikonda abale awo, kuwasamalira komanso kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” w23.09 41:13-14
Lachitatu, July 16
Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.—1 Akor. 3:20.
Tizipewa kuchita zinthu potengera nzeru za anthu. Tikamaona zinthu potengera nzeru za anthu, tingasiye kutsatira mfundo za Yehova. (1 Akor. 3:19) Nthawi zambiri “nzeru za m’dzikoli” zimachititsa kuti anthu asamamvere Mulungu. Akhristu ena a ku Pegamo ndi Tiyatira anayamba kumaona nkhani yokhudza kulambira mafano komanso chiwerewere ngati mmene anthu ambiri m’mizindayo ankaonera. Yesu anadzudzula mwamphamvu mipingo imeneyi chifukwa cholekerera khalidwe la chiwerewere. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso timakakamizidwa kuti tiziona zinthu molakwika. Achibale kapenanso anzathu angatikakamize kapena kutilimbikitsa kuti tichite zinthu zimene zingachititse kuti tisamvere Yehova. Mwachitsanzo, iwo angamatiuze kuti palibe vuto kuchita zomwe tikufuna komanso kuti mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino n’zachikale. Nthawi zina tingamaone kuti malangizo amene Yehova amatipatsa ndi osathandiza. Mwinanso mpaka tikhoza kuyesedwa kuti ‘tipitirire zinthu zolembedwa.’—1 Akor. 4:6. w23.07 31:10-11
Lachinayi, July 17
Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, ankafunika kulimbikitsidwa. Iye sanali pabanja, koma mngelo anamuuza kuti adzakhala ndi pakati. Analinso asanalerepo mwana, koma ankafunika kusamalira mwana yemwe adzakhale Mesiya. Komanso popeza anali asanagonepo ndi mwamuna, kodi akanamufotokozera bwanji Yosefe, yemwe ankayembekezera kukhala naye pabanja? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Iye anadalira ena kuti amuthandize. Mwachitsanzo, anapempha Gabirieli kuti amufotokozere zambiri zokhudza utumikiwu. (Luka 1:34) Pambuyo pake, iye anapita kwa wachibale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe ankakhala “kudera lamapiri” la Yuda. Ulendo umenewu unali wothandiza kwambiri. Elizabeti anayamikira Mariya ndipo mouziridwa ndi Yehova, anamufotokozera ulosi wokhudza mwana yemwe adzabadweyo. (Luka 1:39-45) Mariya ananena kuti Yehova ‘wamuchitira zamphamvu ndi dzanja lake.’ (Luka 1:46-51) Yehova anapatsa mphamvu Mariya pogwiritsa ntchito Gabirieli ndi Elizabeti. w23.10 43:10-12