Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachitatu, July 16

Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.​—1 Akor. 3:20.

Tizipewa kuchita zinthu potengera nzeru za anthu. Tikamaona zinthu potengera nzeru za anthu, tingasiye kutsatira mfundo za Yehova. (1 Akor. 3:19) Nthawi zambiri “nzeru za m’dzikoli” zimachititsa kuti anthu asamamvere Mulungu. Akhristu ena a ku Pegamo ndi Tiyatira anayamba kumaona nkhani yokhudza kulambira mafano komanso chiwerewere ngati mmene anthu ambiri m’mizindayo ankaonera. Yesu anadzudzula mwamphamvu mipingo imeneyi chifukwa cholekerera khalidwe la chiwerewere. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso timakakamizidwa kuti tiziona zinthu molakwika. Achibale kapenanso anzathu angatikakamize kapena kutilimbikitsa kuti tichite zinthu zimene zingachititse kuti tisamvere Yehova. Mwachitsanzo, iwo angamatiuze kuti palibe vuto kuchita zomwe tikufuna komanso kuti mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino n’zachikale. Nthawi zina tingamaone kuti malangizo amene Yehova amatipatsa ndi osathandiza. Mwinanso mpaka tikhoza kuyesedwa kuti ‘tipitirire zinthu zolembedwa.’​—1 Akor. 4:6. w23.07 31:10-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachinayi, July 17

Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.​—Miy. 17:17.

Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, ankafunika kulimbikitsidwa. Iye sanali pabanja, koma mngelo anamuuza kuti adzakhala ndi pakati. Analinso asanalerepo mwana, koma ankafunika kusamalira mwana yemwe adzakhale Mesiya. Komanso popeza anali asanagonepo ndi mwamuna, kodi akanamufotokozera bwanji Yosefe, yemwe ankayembekezera kukhala naye pabanja? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Iye anadalira ena kuti amuthandize. Mwachitsanzo, anapempha Gabirieli kuti amufotokozere zambiri zokhudza utumikiwu. (Luka 1:34) Pambuyo pake, iye anapita kwa wachibale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe ankakhala “kudera lamapiri” la Yuda. Ulendo umenewu unali wothandiza kwambiri. Elizabeti anayamikira Mariya ndipo mouziridwa ndi Yehova, anamufotokozera ulosi wokhudza mwana yemwe adzabadweyo. (Luka 1:39-45) Mariya ananena kuti Yehova ‘wamuchitira zamphamvu ndi dzanja lake.’ (Luka 1:46-51) Yehova anapatsa mphamvu Mariya pogwiritsa ntchito Gabirieli ndi Elizabeti. w23.10 43:10-12

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachisanu, July 18

[Anatipanga] kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake.​—Chiv. 1:6.

Pali ophunzira ochepa a Khristu adzozedwa ndi mzimu woyera, okwana 144,000 omwe ali pa ubwenzi wapadera ndi Yehova. Anthu amenewa adzatumikira ngati ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 1:6; 14:1) Malo Oyera a chihema amaimira kuti iwowa atengedwa kukhala ana auzimu a Mulungu pa nthawi imene ali padziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyera Koposa amaimira kumwamba, komwe Yehova amakhala. “Nsalu,” imene inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa imaimira thupi la Yesu limene linali ngati chotchinga chomulepheretsa kupita kumwamba kukatumikira ngati Mkulu wa Ansembe wapamwamba m’kachisi wauzimu. Yesu atapereka thupi lake ngati nsembe yopulumitsira anthu, anatsegula njira yoti Akhristu onse odzozedwa akakhale ndi moyo kumwamba. Iwonso amafunika kusiya thupi lomwe ali nalo padzikoli kuti akalandire mphoto yawo kumwamba.—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 45:13

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani