NYIMBO 81
Moyo wa Mpainiya
zosindikizidwa
1. M’mawa uliwonse, tulo tisanathe,
Timadzuka n’kupita
kolalikira uthenga.
Ndipo Mulungu amatitsogolera
Timakondwa anthu
akamamvetsera uthenga.
(KOLASI)
Tinasankha,
kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitirizabe kulalikiraku,
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
2. Pofika madzulo, timatopa ndithu,
Komabe timapeza
chimwemwe potumikira.
Madalitso Yehova amatipatsa
Nthawi zonse
timamuthokoza potithandiza.
(KOLASI)
Tinasankha,
kutumikira Yehova.
Timachita zofuna zake.
Tipitirizabe kulalikiraku,
Tikatero timasonyeza
Chikondi.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 92:2; Aroma 14:8.)