NYIMBO 86
Tikhale Anthu Ophunzitsidwa
zosindikizidwa
1. Bwerani mosangalala muphunzire.
“Bwerani m’dzamwe madzi a moyo.”
Dzadyeni inu nonse anjala.
Mudzalandiretu malangizo.
2. Tisaleketu kusonkhana pamodzi,
Tiziphunzitsidwa ndi Mulungu.
Kuno n’kumene kuli abale,
Kuno kulitu mzimu wa M’lungu.
3. Lilime lophunzitsidwa choonadi.
N’losangalatsa kulimvetsera,
Tipezeke ndi anthu a M’lungu,
Tizipezeka pamisonkhano.
(Onaninso Aheb. 10:24, 25; Chiv. 22:17.)