NYIMBO 101
Tizigwira Ntchito Mogwirizana
zosindikizidwa
1. M’dziko logawikanali,
Tili m’gulu la Mulungu.
Timakhala mwamtendere,
N’zosangalatsadi.
Timaunyadira
Mgwirizanowu.
Palitu ntchito yambiri.
Yesu akutsogolera.
Ndiyetu tizimumvera,
N’kumagwirizana.
2. Popempherera umodzi,
Tizikondana kwambiri,
Chikondicho chidzakula,
Komanso mtendere.
Mtendere n’ngwabwino,
Utsitsimula.
Pamene tikukondana,
M’lungu adzatithandiza.
Kukhala ogwirizana,
Pomutumikira.
(Onaninso Mika 2:12; Zef. 3:9; 1 Akor. 1:10.)