NYIMBO 66
Lengezani Uthenga Wabwino
zosindikizidwa
1. Poyamba sitinkadziwa za Ufumu.
Pano tikudziwa Mfumu yalonjezo.
Mwa chifundo ndi chikondi cha Yehova,
Anaganizira anthu ochimwafe.
Anakonza zoti Yesu alamule;
Ufumuwo unali
woti udzabadwe.
Komanso kusankha kagulu ka nkhosa,
Kadzakhale mkwatibwi wa Mwana wake.
2. Mulungu ankadziwa za uthengawu.
Pano akufuna anthu audziwe.
Angelo amakondwa potithandiza
Kugwira ntchito yolengeza Ufumu.
Tilitu ndi udindo ndiponso mwayi
Wom’tamanda ndi kuyeretsa
dzina lake.
Tili ndi mwayi wolengeza dzinalo
Mwa kulalikira uthenga wabwino.
(Onaninso Maliko 4:11; Mac. 5:31; 1 Akor. 2:1, 7.)