CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 13-14
“Chilimikani ndi Kuona Chipulumutso cha Yehova”
Yehova ndi Mpulumutsi amene amaganizira anthu ake. Kodi anasonyeza bwanji kuti ankaganizira kwambiri Aisiraeli pamene ankachoka ku Iguputo?
Anawathandiza kuyenda mwadongosolo.—Eks 13:18
Ankawatsogolera komanso kuwateteza.—Eks 14:19, 20
Anapulumutsa anthu ake onse, kuyambira ana mpaka achikulire.—Eks 14:29, 30
Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani pamene chisautso chachikulu chikuyandikira?—Yes 30:15