NYIMBO 143
Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso ndi Kudikira
zosindikizidwa
1. Nthawi ya Mulungu wathu,
Yayandikira kwambiri—
Kutitu alamulire
Umboni waoneka.
(KOLASI)
Pitirizani kukhala maso,
Kuti mudzapeze moyo,
Womwe M’lungu wakonza.
2. M’lungu anaika nthawi;
Yoti Yesu agonjetse,
Adani ake onsewa.
Iye adzapambana.
(KOLASI)
Pitirizani kukhala maso,
Kuti mudzapeze moyo,
Womwe M’lungu wakonza.
3. Mavuto m’chilengedwechi,
Akuchuluka kwambiri.
Tiyembekeze Yehova,
Adzatipulumutsa.
(KOLASI)
Pitirizani kukhala maso,
Kuti mudzapeze moyo,
Womwe M’lungu wakonza.
(Onaninso Mat. 25:13; Luka 12:36.)