NYIMBO 79
Athandizeni Kukhala Olimba
zosindikizidwa
1. Kuphunzitsa nkhosa za M’lungu
Ndi mwayi wapadera.
Yehova wawatsogolera
Amakonda cho’nadi.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
2. Mayesero akawagwera,
Tinkawapempherera.
Tinawaphunzitsa mwakhama;
Pano adalitsidwa.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
3. Akhale okudalirani,
Inu M’lungu ndi Yesu.
Apirire pamayesero,
Akalandire moyo.
(KOLASI)
Yehova tikupemphatu
Kuti muziwateteza.
Mwa Yesu tikupemphani: Athandizenibe
Akhale olimba.
(Onaninso Luka 6:48; Mac. 5:42; Afil. 4:1.)