NYIMBO 144
Yang’ananibe Pamphoto
zosindikizidwa
1. Pomwe osaona ’kuwona
Ovutika kumva akumva,
Ana adzaimbanso nyimbo,
Mtendere padziko lonse,
Omwe anafa adzauka,
Uchimo, mavuto zathanso,
(KOLASI)
Mudzaona zinthu zonsezi,
M’kayang’anabe pamphoto.
2. Mimbulu idzadya ndi nkhosa,
Zilombo zoopsa ndi ng’ombe,
Mwana adzazitsogolera,
Zidzamvera mawu ake.
Pamene misozi idzatha,
Mantha ndi zowawa zathanso,
(KOLASI)
Mudzaona zinthu zonsezi,
M’kayang’anabe pamphoto.
(Onaninso Yes. 11:6-9; 35:5-7; Yoh. 11:24.)