NYIMBO 108
Chikondi Chosatha cha Mulungu
zosindikizidwa
1. M’lungu ndi chikondi.
Amatikonda kwambiri.
Anaperekatu Yesu
N’kuwombola anthu tonse,
Timayembekezeranso
Moyo wosangalatsadi.
(KOLASI)
Inu nonse a ludzu,
Dzamweni kwaulere.
Madzi opatsa moyo;
Mulungu n’chikondi.
2. M’lungu ndi chikondi.
Ntchito zake ndi umboni.
Wasonyezanso chikondi,
Popatsa Yesu Ufumu.
Ufumu wa Yesu pano.
Wayamba kulamulira.
(KOLASI)
Inu nonse a ludzu,
Dzamweni kwaulere.
Madzi opatsa moyo;
Mulungu n’chikondi.
3. M’lungu ndi chikondi.
Nafenso tichisonyeze.
Pothandiza ’nthu ofatsa,
Kusungatu malamulo.
Timamvera M’lungu wathu,
Tilalikira konseko.
(KOLASI)
Inu nonse a ludzu,
Dzamweni kwaulere.
Madzi opatsa moyo;
Mulungu n’chikondi.
(Onaninso Sal. 33:5; 57:10; Aef. 1:7.)