Kodi Nyonga Yawo Amaipeza Kuti?
MUTAYANG’ANITSITSA gulugufe pachithunzithunzi ichi, mudzaona kuti limodzi la mapiko ake anayi nlotheratu ntchito. Komabe, gulugufe ameneyu amapitirizabe kudya ndi kuuluka. Sindiye yekha amene ali wotere. Agulugufe aonedwa akuchita ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku alibe 70 peresenti ya mbali zawo za mapiko.
Momwemonso, anthu ambiri amasonyeza mzimu wakulimbika mtima. Ngakhale kuti amavutika kwambiri ndi zovuta za m’thupi kapena kupsinjika, iwo safooka.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:16.
Mtumwi Paulo iye yekha anapirira zovuta zazikulu pamaulendo ake aumishonale. Anakwapulidwa, kumenyedwa, kuponyedwa miyala, ndi kuikidwa m’ndende. Ndiponso, anali ndi chilema china chake, mwinamwake vuto la maso ake limene kwa iye linali “munga m’thupi” nthaŵi zonse.—2 Akorinto 12:7-9; Agalatiya 4:15.
Mkulu wachikristu wotchedwa David, amene analimbana ndi kuchita tondovi kwa zaka zambiri, akhulupirira kuti nyonga ya Yehova inathandiza kwambiri kuchira kwake. “Nthaŵi ndi nthaŵi, kupita patsogolo kumene ndinachita movutikira kunaoneka ngati kukuzimirira,” iye akutero. “Polimbana ndi kulefuka kumeneko, ndinadalira Yehova kotheratu, ndipo anandichirikizadi. Nthaŵi zina ndinali kupemphera maola ambiri nthaŵi imodzi. Pamene ndinalankhula ndi Yehova, kusungulumwa kwanga ndi maganizo akudziyesa wachabe zinazimiririka. Ndalimbikira panyengo zakufooka kwakukulu, koma ndi thandizo la Yehova, ndapeza nyonga m’kufooka kumeneku—ngakhale nyonga yothandiza nayo ena.”
Yehova Mulungu anapatsa Paulo nyonga. Chifukwa chake, iye anatha kunena kuti: “Pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:10) Inde, kufooka kwa Paulo kunamphunzitsa kudalira nyonga yoperekedwa ndi Mulungu. “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo,” anatero mtumwiyo. (Afilipi 4:13) Ndithudi Yehova amaperekadi mphamvu kwa atumiki ake.