Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 6 tsamba 9
  • Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mphotho ya Yobu—Magwero a Chiyembekezo
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 6 tsamba 9
Yobu ali ndi zilonda pathupi lake

GAWO 6

Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika

Satana anatsutsa zoti Yobu amatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, koma Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova

KODI pali munthu aliyense amene angakhalebe wokhulupirika kwa Mulungu ngati atayesedwa kwambiri ndiponso ngati zikuoneka kuti sakupindulapo chilichonse mwakuthupi chifukwa chokhala womvera? Zimene zinachitika pa moyo wa Yobu zinali zokhudza funso limeneli, ndipo iye analiyankha.

Pamene Aisiraeli anali ku Iguputo, Yobu amene anali m’bale wake wa Abulahamu, ankakhala m’dziko limene panopa limatchedwa Arabia. Nthawi ina angelo anasonkhana pamaso pa Mulungu kumwamba, ndipo Satana anali pomwepo. Pamaso pa angelo onsewo, Yehova anasonyeza kuti amakhulupirira mtumiki wake wokhulupirika Yobu. Ndipotu Yehova ananena kuti panalibe munthu wina amene ankamutumikira ndi mtima wosagawanika kuposa Yobu. Koma Satana ananena kuti Yobu amatumikira Mulungu chifukwa chakuti Mulunguyo anamudalitsa ndiponso amamuteteza. Satana ananena kuti ngati Yobu atalandidwa chilichonse chimene anali nacho, angatukwane Mulungu.

Angelo akuonekera pamaso pa Mulungu kumwamba ndipo Satana alinso pomwepo

Mulungu analola kuti Satana awononge chuma cha Yobu, achititse kuti ana ake afe ndiponso kuti amudwalitse. Yobu sankadziwa kuti Satana ndi amene anachititsa mayesero amene ankakumana nawo, choncho sankamvetsa chifukwa chimene Mulungu analolera kuti iye azivutika. Komabe, Yobu sanatukwane Mulungu.

Anthu atatu amene ankaoneka ngati anzake a Yobu anabwera. M’masamba ambiri a buku la Yobu muli mawu a anthu amenewa. Iwo anali ndi maganizo olakwika ndipo anayesa kutsimikizira Yobu kuti Mulungu akumulanga chifukwa cha machimo enaake obisika amene iye anachita. Iwo ananenanso kuti Mulungu sasangalala ndi atumiki ake komanso sawakhulupirira. Koma Yobu anatsutsa maganizo awo olakwikawo, ndipo molimba mtima ananena kuti apitirizabe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa yake.

Koma Yobu analakwitsa zinthu chifukwa ankadziona ngati wolungama kwambiri. Choncho munthu wina wachinyamata wotchedwa Elihu amene ankamvetsera zonse zimene Yobu ndi anthu atatuwo ankakambirana, anadzudzula Yobu ndi anzakewo. Elihu anadzudzula Yobu chifukwa sanazindikire msanga kuti ulamuliro wa Yehova Mulungu ndiye woyenera kukwezedwa osati kukweza munthu wina aliyense. Komanso anadzudzula mwamphamvu anzake a Yobu aja omwe anali onyenga.

Kenako Yehova Mulungu analankhula ndi Yobu ndi kumuthandiza kuchotsa maganizo ake olakwikawo. Yehova anatchula zinthu zambiri zodabwitsa za m’chilengedwe pothandiza Yobu kuona kuti munthu ndi wamng’ono kwambiri pomuyerekezera ndi Mulungu. Yobu analandira modzichepetsa malangizo ochokera kwa Mulungu. Yehova, amene ndi “wachikondi chachikulu ndi wachifundo,” anachiritsa Yobu, anachulukitsa chuma chake kawiri poyerekezera ndi chimene anali nacho poyamba ndiponso anamudalitsa pomupatsa ana 10. (Yakobo 5:11) Popitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wosagawanika pa nthawi ya mayesero aakulu, Yobu anayankha bodza limene Satana ananena lakuti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati atakumana ndi mayesero.

​—Nkhaniyi yachokera m’buku la Yobu.

  • Kodi Satana anatsutsa chiyani pa nkhani ya Yobu?

  • Kodi Yobu anayankha bodza liti pamene anapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wosagawanika?

NKHANI ZOFUNIKA KWAMBIRI

Ponena kuti Yobu akutumikira Yehova Mulungu chifukwa cha dyera basi, Satana anatanthauza kuti anthu onse komanso angelo amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Yobu anali munthu wosalakwa komanso anali woopa Mulungu kwambiri kuposa wina aliyense padziko lapansi pa nthawiyo. Pamenepa Satana anakayikira zoti anthu angatumikiredi Yehova ndi mtima wosagawanika. Imeneyi ndi mbali ya nkhani yonse imene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni. Iye anakayikira zoti Yehova ndi woyenera kulamulira komanso zoti amalamulira mwachilungamo. Buku la Yobu limasonyeza kuti angelo ndiponso anthu angathandize kukweza ulamuliro wa Yehova pomutumikira ndi mtima wosagawanika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena