Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 100
  • Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene simuyenera kuchita
  • Zimene zingathandize
  • Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kusangalalako?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Anandiikira Malamulo Ambirimbiri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikhulupirira?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 100
Makolo akulankhula ndi mwana wawo yemwe wafika panyumba mochedwa.

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?

Pafupifupi banja lililonse limakhala ndi malamulo, mwina okhudza zinthu ngati nthawi yofikira kunyumba, kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kapena makhalidwe abwino.

Koma kodi mungatani ngati mwaphwanya lamulo linalake? Simungasinthe zimene zachitika koma mungathandize kuti zinthu zisaipe kwambiri. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite.

  • Zimene simuyenera kuchita

  • Zimene zingathandize

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Zimene simuyenera kuchita

  • Ngati makolo anu sakudziwa kuti simunatsatire lamulo linalake, mwina mungafune kubisa zimene mwachita.

  • Ngati akudziwa kuti simunamvere lamulolo, mwina mungafune kupereka zifukwa zodzikhululukira kapena kuloza chala munthu wina.

Si nzeru kuchita zinthu zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Zili choncho chifukwa chakuti kubisa zimene mwachita kapena kupereka zifukwa zodzikhululukira n’zachibwana. Zikhoza kuchititsa makolo anu kuganiza kuti simunafike pokhala munthu wodalirika.

“Si bwino kunama. Pakapita nthawi, zoona zake zidzadziwika ndipo chilango chimene udzapatsidwa chidzakhala chokhwima kwambiri kuposa chimene ukanalandira ngati ukanangonena zoona zake poyamba.”—Diana.

Zimene zingathandize

  • Muzivomereza zimene mwalakwitsa. Baibulo limanena kuti: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino.” (Miyambo 28:13) Makolo anu amadziwa kuti si inu wangwiro. Koma funso n’kumati, Kodi mumachita zinthu moona mtima?

    “Makolo adzakuchitira chifundo ngati unena zoona zake. Ukavomereza zimene wachita, adzayamba kukhulupirira kuti ndiwe woona mtima komanso wokhulupirika.”—Olivia.

  • Muzipepesa. Baibulo limanena kuti: “Muzichitirana zinthu modzichepetsa.” (1 Petulo 5:5) Kunena kuti “pepani” komanso kupewa kupereka zifukwa zodzikhululukira kumafuna kudzichepetsa.

    “Anthu amene nthawi zonse amapereka zifukwa zodzikhululukira akhoza kuwononga chikumbumtima chawo. Kenako akhoza kusiyiratu kudziimba mlandu akachita zinthu zoipa.”—Heather.

  • Muzivomereza chilango chimene mwalandira. Baibulo limanena kuti: “Mverani malangizo.” (Miyambo 8:33) Muzipewa kudandaula ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi chilango chimene makolo anu akupatsani.

    “Ukamangodandauladandaula ndi chilango chimene walandira, zinthu zikhoza kuipa kwambiri. Uziyesetsa kungovomereza chilangocho m’malo mochiganizira kwambiri.”—Jason.

  • Muziyesetsa kukhala wodalirika. Baibulo limanena kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” (Aefeso 4:22) Muyambe kuchita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodalirika.

    “Nthawi zonse ukamayesetsa kusankha zochita mwanzeru n’kumasonyeza makolo ako kuti sudzachitsanso zimene unalakwitsazo, iwo adzayambanso kukukhulupirira.”—Karen.

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Muzichita zonse zimene mungathe posonyeza kuti ndinu wodalirika. Mwachitsanzo, mukachoka pakhomo, muziuza makolo pamene muli m’njira yobwerera kunyumba ngakhale ngati simufika mochedwa. Izi zingawasonyeze kuti mukufuna kuti iwo azikukhulupirirani.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Darius.

“Ukabisira makolo zimene wachita umakhala ukunama. Pakapita nthawi, zimene wachita zidzadziwika ndipo zinthu sizidzakuyendera bwino ngati mmene zikanachitira ngati ukangonena zoona zake poyamba.”—Darius.

Sierra.

“Tikamaimba mlandu anthu ena chifukwa cha zimene tachita, timaoneka kuti sitinafike pokhala munthu amene angavomereze zimene walakwitsa. Makolo athu angasiye kutikhulupirira ngati sitipepesa tikalakwitsa zinthu.”—Sierra.

Mfundo zobwereza: Kodi Ndingatani Ngati Ndaphwanya Lamulo la Makolo Anga?

  • Muzivomereza zimene mwalakwitsa. Makolo anu amadziwa kuti si inu wangwiro. Koma funso n’kumati, Kodi ndinu woona mtima?

  • Muzipepesa. Muzinena kuti “pepani” ndipo muzipewa kupereka zifukwa zodzikhululukira.

  • Muzivomereza chilango chimene mwalandira. Muzichita zinthu mogwirizana ndi chilango chimene makolo angakupatseni.

  • Muziyesetsa kukhala wodalirika. Muyambe kuchita zinthu zimene zingasonyeze kuti ndinu wodalirika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena