Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 44
  • Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
  • Kodi zoona zake n’zotani?
  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?
  • Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira pa Nkhani ya Kugonana?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kugonana?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Muzikambirana ndi Ana Anu Nkhani Zokhudza Kugonana
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Bwanji Zolumbira Kukhala Odzisunga?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 44
Chithunzi cha mnyamata ndi mtsikana

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?

Bungwe lina la ku United States linachita kafukufuku n’kupeza kuti pa achinyamata azaka pakati pa 15 ndi 19 omwe anawafunsa, pafupifupi hafu anali atagonanapo m’kamwa. Munthu wina amene analemba buku lokhudza kugonana m’kamwa dzina lake Sharlene Azam anati: “Mukafunsa achinyamata za [kugonana m’kamwa] amanena kuti si nkhani yaikulu. Iwo amaona kuti si kugonana kwenikweni.”

  • Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

  • Kodi zoona zake n’zotani?

  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Yankhani mafunso otsatirawa kuti inde kapena ayi.

  1. Kodi mtsikana angatenge mimba chifukwa chogonana m’kamwa?

    1. Inde

    2. Ayi

  2. Kodi kugonana m’kamwa kungayambitse matenda?

    1. Inde

    2. Ayi

  3. Kodi kugonana m’kamwa kumakhaladi kugonana?

    1. Inde

    2. Ayi

Kodi zoona zake n’zotani?

Yerekezerani mayankho anu ndi amene ali m’munsiwa.

  1. Kodi mtsikana angatenge mimba chifukwa chogonana m’kamwa?

    Yankho: Ayi. N’chifukwa chake anthu ambiri amaganiza molakwika kuti kugonana m’kamwa sikungabweretse mavuto.

  2. Kodi kugonana m’kamwa kungayambitse matenda?

    Yankho: Inde. Anthu amene amagonana m’kamwa angayambe kudwala matenda a chiwindi (hepatitis A kapena B), njerewere za kumaliseche, chinzonono, mabomu, edzi ndi chindoko.

  3. Kodi kugonana m’kamwa kumakhaladi kugonana?

    Yankho: Inde. Kugonana kumaphatikizapo kugonana m’kamwa, kugonana kumatako komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina.

Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

Ganizirani malemba ena m’Baibulo amene amakhudza nkhani ya kugonana m’kamwa.

Baibulo limati: ‘Mulungu akufuna kuti mupewe dama.’—1 Atesalonika 4:3.

Mawu oyambirira amene anawamasulira kuti “dama,” akutanthauza kugonana, kugonana m’kamwa, kugonana kumatako kapena kuseweretsa maliseche a munthu wina ndipo akutanthauza kuchita zinthuzi ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu. Munthu amene amachita dama angakumane ndi mavuto ambiri. Koma vuto lalikulu n’lakuti akhoza kuwononga ubwenzi wake ndi Mulungu.​—1 Petulo 3:12.

Baibulo limati: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.”—1 Akorinto 6:18.

Munthu akhoza kudwala, kuwononga ubwenzi wake ndi Yehova komanso kusokonezeka maganizo chifukwa chogonana m’kamwa. Buku lina limati: “Munthu akagonana ndi munthu wina amene sayenera kugonana naye akhoza kudandaula ndiponso kunong’oneza bondo pambuyo pake. Izi zimakhala choncho ngakhale kuti munthuyo wagonana m’njira ina monga m’kamwa. Mtundu uliwonse wa kugonana ndi kugonana basi.”—Talking Sex With Your Kids.

Baibulo limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17.

Kodi mumakhulupirira kuti malamulo a Mulungu okhudza kugonana ndi othandizadi? Kapena kodi mumaona kuti malamulowo ndi ovuta? Kuti muyankhe mafunsowa, ganizirani za msewu waukulu umene mumadutsa magalimoto ambiri. Pamsewuwu pamakhala zikwangwani zokuuzani liwiro limene muyenera kuyenda kapena pamene muyenera kuima. Pamakhalanso maloboti okuuzani pamene muyenera kuima kapena kupita. Kodi mumaona kuti zinthuzi zimakutetezani kapena zimakuletsani kuchita zimene mukufuna? Nanga n’chiyani chingachitike ngati inuyo kapena anthu ena atangozinyalanyaza?

Woyendetsa galimoto wanyalanyaza chikwangwani chapamsewu ndipo walowa m’njira yolakwika

Malamulo apamsewu amakuletsani kuchita zinthu zina koma amakutetezani. Nawonso malamulo a Mulungu amachita zimenezi

N’chimodzichimodzi ndi malamulo a Mulungu. Mukangowanyalanyaza mumakolola zimene mwafesa. (Agalatiya 6:7) Buku lina limati: “Mukamachita zinthu zotsutsana ndi zimene mumakhulupirira kapena zimene mumadziwa kuti ndi zoyenera, mumayamba kudzimva kuti ndinu opanda pake.” (Sex Smart) Koma munthu amene amatsatira mfundo za Mulungu, sadziimba mlandu ndipo anthu ena amamulemekeza.—1 Petulo 3:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena