Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 75
  • Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene muyenera kudziwa
  • Zimene mungachite
  • N’chifukwa Chiyani Mnzanga Wayamba Kudana Nane?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • N’chifukwa Chiyani Bwenzi Langa Linandikhumudwitsa?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Kukhululuka Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Musamakhumudwitse “Tianati”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 75
Mtsikana walankhula mawu omwe akhumudwitsa mnzake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

  • Zimene muyenera kudziwa

  • Zimene mungachite

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Zimene muyenera kudziwa

  • Tonse tikhoza kukhumudwitsa anzathu. Mnzanu wapamtima kapenanso aliyense amene mumamuona ngati mnzanu, akhoza kulankhula kapena kuchita zinthu zina zomwe zingakukhumudwitseni chifukwa ndi munthu wopanda ungwiro. Ndiye popeza inunso ndinu wopanda ungwiro, kodi munganene kuti simunayambe mwakhumudwitsapo anzanu?​—Yakobo 3:2.

  • Zomwe zimaikidwa pa intaneti zingachititsenso kuti mukhumudwe. Mwachitsanzo mnyamata wina dzina lake David ananena kuti: “Ukatsegula intaneti n’kuona chithunzi chosonyeza kuti mnzako anali ku pate kwinakwake, umayamba kudabwa kuti n’chifukwa chiyani sanandiitane. Zikatero umakhumudwa ndipo umangoona ngati akutaya.”

  • Mukhoza kuthana ndi vutoli.

Zimene mungachite

Mudzifufuze. Baibulo limati: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”​—Mlaliki 7:9.

Alyssa ananena kuti: “Nthawi zina pakapita masiku m’pamene umaona kuti unangokhumudwa ndi zazing’ono.”

Zoti muganizire: Kodi mumangokhumudwa zilizonse? Kodi pali zimene mungachite kuti musamakhumudwe kwambiri ndi zomwe anzanu amachita?​—Mlaliki 7:21, 22.

Muziganizira kufunika kokhululukira ena. Baibulo limati: ‘Kunyalanyaza cholakwa kumachititsa [munthu] kukhala wokongola.’​—Miyambo 19:11.

Mallory ananena kuti: “Ngakhale utakhumudwa pa zifukwa zomveka, ndi bwino kukhululuka ndi mtima wonse. Ukatero siufunikanso kumangokumbutsa mnzakoyo zomwe analakwitsa kuti azingokhalira kukupepesa. Ukamukhululukira, nkhaniyo izitheranso pomwepo.”

Zoti muganizire: Kodi ndi nkhani yaikuludi? Kodi mungathe kungomukhululukira kuti mukhalenso pamtendere?​—Akolose 3:13.

Kulowetsa mphepo yozizira m’nyumba moti mukutenthera

Kumangokhalira kulankhula zomwe mnzanu anakulakwirani, kuli ngati kulowetsa mphepo yozizira m’nyumba moti mukutenthera.

Muziganizira zofuna za mnzanuyo. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:4.

Nicole ananena kuti: “Mukamakondana komanso kulemekezana, mumayesetsa kuti mugwirizanenso mwamsanga mukasemphana zochita. Mumakhala kuti munachitira limodzi zinthu zambiri choncho simungafune kuti musiyane.”

Zoti muganizire: Kodi mungathe kumvetsa chifukwa chimene chachititsa mnzanuyo kulankhula kapena kuchita zinthu zimenezo?​—Afilipi 2:3.

Mfundo yofunika kwambiri: Muyenera kudziwiratu zimene mungachite anzanu akakukhumudwitsani ndipo zimenezi zidzakuthandizani mukadzakula. Yesetsani kuphunzira kuchita zimenezi panopa.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Kiana

Kiana ananena kuti: “Si nkhani zonse zomwe umafunika kuzikoka. Zina umafunika kungozimwera madzi basi. Zimenezi zimathandiza kuti ukhale pamtendere ndi anzako.”

Treigh

Treigh ananenanso kuti: “Pakabuka nkhani inayake, ndimadzifunsa kaye ngati ilidi nkhani yaikulu yoti mpaka ndingasiye kucheza ndi mnzangayo. Ndimaona kuti nthawi zambiri sizikhala nkhani zodetsa nkhawa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena