Genesis 21:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri n’kutenga mkate ndi thumba la madzi lachikopa, n’kuziika paphewa pa Hagara.+ Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Chotero Hagarayo ananyamuka n’kumangoyendayenda m’chipululu cha Beere-seba.*+ Yohane 8:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Komanso, kapolo sakhala m’banjamo kwamuyaya, mwana ndiye amakhalamo kwamuyaya.+ Agalatiya 4:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, pakuti sizingatheke mwana wa mdzakazi kudzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi waufulu.”+
14 Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri n’kutenga mkate ndi thumba la madzi lachikopa, n’kuziika paphewa pa Hagara.+ Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Chotero Hagarayo ananyamuka n’kumangoyendayenda m’chipululu cha Beere-seba.*+
30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, pakuti sizingatheke mwana wa mdzakazi kudzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi waufulu.”+