Deuteronomo 11:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma dziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Ilo limamwa madzi a mvula, madzi ochokera kumwamba. Yesaya 45:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Inu kumwamba, chititsani chilungamo kuvumba ngati mvula.+ Kumwamba kwa mitambo kuchuche chilungamo.+ Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso. Lichititse chilungamo kuphuka+ pa nthawi imodzimodziyo. Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”+ Hoseya 14:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,+ ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola. Mizu yake idzazama ngati mtengo wa ku Lebanoni.
11 Koma dziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Ilo limamwa madzi a mvula, madzi ochokera kumwamba.
8 “Inu kumwamba, chititsani chilungamo kuvumba ngati mvula.+ Kumwamba kwa mitambo kuchuche chilungamo.+ Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso. Lichititse chilungamo kuphuka+ pa nthawi imodzimodziyo. Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”+
5 Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,+ ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola. Mizu yake idzazama ngati mtengo wa ku Lebanoni.