9 Ineyo ndikhala chikole cha moyo wa mnyamatayu.+ Chilangocho chikabwere pa ine.+ Ndikadzalephera kubwera naye ndi kum’pereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse.
32 Ine kapolo wanu ndinadzipereka kukhala chikole+ cha moyo wa mwanayu pamene ali kutali ndi bambo ake. Ndinalonjeza kuti, ‘Ndikadzalephera kubwera naye kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu bambo anga moyo wanga wonse.’+