19 Yehova Mulungu anali kuumba ndi dothi nyama iliyonse yakutchire, ndi cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga. Ndipo anayamba kuzibweretsa kwa munthuyo, kuti chilichonse achitche dzina. Dzina lililonse limene munthuyo anatchula chamoyo chilichonse,+ limenelo linakhaladi dzina lake.+