11 Akanani amene anali kukhala m’dzikolo anaona miyambo yolirira maliro imene inali kuchitikira pamalo opunthira mbewu a Atadi. Ataona choncho, iwo anati: “Maliro amene agwera Aiguputowa ndi aakulu!” N’chifukwa chake malowo anawatcha Abele-miziraimu, ndipo ali m’chigawo cha Yorodano.+