8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+