13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzaleka kuwapitikitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu.+ Adzakhalanso ngati zokubayani m’mbali mwanu komanso ngati zitsotso m’maso mwanu, kufikira mutatheratu padziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+