Ekisodo
23 “Usafalitse nkhani yabodza.+ Usagwirizane ndi munthu woipa mwa kukhala mboni yokonzera wina zoipa.+ 2 Usatsatire khamu pochita zoipa.+ Pa mlandu usapereke umboni wopotoza chilungamo potsatira khamu la anthu.+ 3 Usakondere munthu wosauka pa mlandu wake.+
4 “Ukapeza ng’ombe kapena bulu wa mdani wako atasochera, um’bweze ndithu kwa mwiniwake.+ 5 Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+
6 “Usapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+
7 “Utalikirane ndi mawu onama.+ Usaphe munthu wosalakwa ndi munthu wolungama, chifukwa woipa sindidzamuyesa wolungama.+
8 “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+
9 “Usapondereze mlendo wokhala pakati panu,+ popeza mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+
10 “Kwa zaka 6 uzilima munda wako ndi kukolola.+ 11 Koma chaka cha 7 usaulime, uusiye kuti ugonere.+ Osauka mwa anthu ako adye za m’mundamo ndipo zimene iwo asiya, zilombo zakutchire zidye.+ Uzichita zimenezi ndi munda wako wa mpesa ndi wa maolivi.
12 “Uzigwira ntchito masiku 6.+ Koma tsiku la 7 usamagwire ntchito, kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zizipuma, ndipo mwana wa kapolo wako wamkazi ndi mlendo azipumula.+
13 “Muzisamalira zonse zimene ndakuuzani,+ ndipo musatchule dzina la milungu ina. Lisamveke pakamwa panu.+
14 “Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15 Muzichita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa+ masiku 7 pa nthawi yake m’mwezi wa Abibu,*+ monga momwe ndakulamulirani, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi umenewu. Ndipo palibe ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+ 16 Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+ 17 Katatu pa chaka mwamuna aliyense pakati panu azionekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+
18 “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Ndipo mafuta a chikondwerero changa asamagone mpaka m’mawa.+
19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+
“Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+
20 “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+ 21 Samala ndipo umvere mawu ake. Usam’pandukire, chifukwa sadzalekerera zolakwa zanu,+ pakuti dzina langa lili mwa iye. 22 Koma ukalabadiradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanena,+ pamenepo ndidzalusira adani ako ndi kuvutitsa okuvutitsa.+ 23 Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+ 24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ 25 Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndipo ndidzachotsa matenda pakati panu.+ 26 M’dziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku anu.+
27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+ 28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+ 29 Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+ 30 Ndidzawathamangitsa pamaso pako pang’onopang’ono kufikira mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+
31 “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+ 32 Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33 Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+