11 Mpandawo kumbali yakumpoto, m’litali mwake ukhalenso momwemo. Nsalu yampandawo ikhale mikono 100 m’litali mwake, ndipo kukhale nsanamira 20 ndi zitsulo zamkuwa 20 zamphako zokhazikapo nsanamirazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi mfundo zake zikhale zasiliva.+