3 Usadye nsembeyo pamodzi ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa. Masiku 7+ uzidya mkate wopanda chofufumitsa, umene ndi mkate wa nsautso, chifukwa unatuluka mofulumira m’dziko la Iguputo.+ Uzichita zimenezi kuti uzikumbukira tsiku limene unatuluka m’dziko la Iguputo, masiku onse a moyo wako.+