Deuteronomo 4:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Choncho anthu inu munayandikira ndi kuimirira m’munsi mwa phiri. Phiri limenelo linali kuyaka moto mpaka kumwamba, ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ Deuteronomo 5:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “Yehova analankhula Mawu* amenewa mokweza kumpingo wanu wonse, kuchokera pakati pa moto m’phiri,+ pamene kunachita mtambo wakuda ndi mdima wandiweyani, ndipo pa Mawuwo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema n’kundipatsa.+ Salimo 68:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+ Salimo 104:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Amayang’ana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.+Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+
11 “Choncho anthu inu munayandikira ndi kuimirira m’munsi mwa phiri. Phiri limenelo linali kuyaka moto mpaka kumwamba, ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+
22 “Yehova analankhula Mawu* amenewa mokweza kumpingo wanu wonse, kuchokera pakati pa moto m’phiri,+ pamene kunachita mtambo wakuda ndi mdima wandiweyani, ndipo pa Mawuwo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema n’kundipatsa.+
8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+