33 Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Nyamukani, muchoke pano, iweyo ndi anthu amene unawatsogolera potuluka m’dziko la Iguputo.+ Mupite kudziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili kwa mbewu yako.’+