18 Ndiyeno tsiku ndi tsiku, kuchokera tsiku loyamba mpaka tsiku lomaliza, anali kuwerenga mokweza buku la chilamulo cha Mulungu woona.+ Iwo anachita chikondwererocho masiku 7, ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera malinga ndi lamulo.+
37 Tsopano pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira ndi kufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu,+ abwere kwa ine adzamwe madzi.