36 Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musagwire ntchito iliyonse yolemetsa.
37 Tsopano pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira ndi kufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu,+ abwere kwa ine adzamwe madzi.