15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi, ndi kutengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, azizitentha paguwa lansembe kuti zikhale fungo la chikumbutso,+ lokhazika mtima pansi, kwa Yehova.