15 Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa+ pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.+