12 Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso ndi Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, kuti: “Tengani nsembe yambewu+ imene yatsala pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda chofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe, chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+