7 Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+