30 Gawo lawo linayambira ku Mahanaimu+ kuphatikizapo dera lonse la Basana,+ ndi dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, ndiponso midzi yonse ing’onoing’ono ya Yairi+ ku Basana. Gawo lawoli linali ndi matauni 60 onse pamodzi.
23 Ana a hafu ya fuko la Manase+ anakhala m’dera loyambira ku Basana+ mpaka ku Baala-herimoni,+ ku Seniri,+ ndi kuphiri la Herimoni,+ ndipo iwo anachulukana kwambiri.