Deuteronomo 9:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 ndipo Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene chala cha Mulungu chinalembapo.+ Pamiyala iwiri imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu m’phiri, kuchokera pakati pa moto, tsiku limene munasonkhana kumeneko.+ Deuteronomo 10:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Pamenepo analemba pamiyalayo mawu ofanana ndi oyamba aja,+ Mawu Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani m’phiri kuchokera pakati pa moto,+ tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo.
10 ndipo Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene chala cha Mulungu chinalembapo.+ Pamiyala iwiri imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu m’phiri, kuchokera pakati pa moto, tsiku limene munasonkhana kumeneko.+
4 Pamenepo analemba pamiyalayo mawu ofanana ndi oyamba aja,+ Mawu Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani m’phiri kuchokera pakati pa moto,+ tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo.