Ekisodo 34:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+ Deuteronomo 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+ Deuteronomo 31:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga!
9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+
6 Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+
27 Pakuti ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma khosi kwanu.+ Ngati lero pamene ndili moyo pamodzi nanu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova,+ ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga!