-
Deuteronomo 12:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndiyeno malo+ amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuti pakhale dzina lake n’kumene muzidzabweretsa zonse zimene ndikukulamulani, nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka+ chochokera m’manja mwanu ndi zonse zimene mwasankha kukhala nsembe zanu za lonjezo,+ zimene mudzalonjeza Yehova.
-
-
Deuteronomo 14:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Uzidzadya zinthu zako pamaso pa Yehova Mulungu wako, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake. Uzidzadya chakhumi cha mbewu zako,+ kumwa vinyo wako watsopano, kudya mafuta ako, ana oyamba a ng’ombe ndi a nkhosa zako.+ Uzichita zimenezi kuti uphunzire kuopa Yehova Mulungu wako nthawi zonse.+
-