19 Zopereka zonse zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova, ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, ngati gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano losatha* limene lidzakhala mpaka kalekale pakati pa Yehova ndi iwe ndi mbadwa zako.”+
6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo.