Deuteronomo 4:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma nonsenu amene mukumamatira+ kwa Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo lero. Deuteronomo 10:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Muziopa Yehova Mulungu wanu.+ Muzim’tumikira,+ kum’mamatira+ ndi kulumbira pa dzina lake.+ Yoswa 23:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma mamatirani+ Yehova Mulungu wanu monga mmene mwakhala mukuchitira kufikira lero.