33 Ana anu adzakhala abusa m’chipululu+ kwa zaka 40, ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika*+ kwanu, mpaka womalizira kufa wa inu atagona m’manda m’chipululu.+
3 Ndiyeno m’chaka cha 40,*+ m’mwezi wa 11, pa tsiku loyamba la mweziwo, Mose analankhula ndi ana a Isiraeli zonse zimene Yehova anamulamula kuti awauze.