20 Ansembe aja ataliza malipenga awo,+ asilikaliwo anafuula. Atangomva kulira kwa malipenga, anayamba kufuula mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wa mzindawo unayamba kugwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko, ndi kulanda mzindawo.