22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe.
13 Kalebe+ mwana wa Yefune anam’patsa gawo lake pakati pa ana a Yuda pomvera lamulo la Yehova kwa Yoswa. Anam’patsa Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali tate wa Anaki.)