-
Oweruza 7:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tsopano Gidiyoni anafika kumsasawo ndipo anangomva munthu akusimbira mnzake zimene analota, kuti: “Tamvera zimene ndalota ine.+ Ndalota mtanda wa mkate wa balere wozungulira ukugubuduzika kubwera mumsasa wa Amidiyani. Mtandawo unafika pahema lina ndi kuliwomba moti hemalo linagwa.+ Kenako mtandawo unagadabuza hemalo n’kuliphwasula.”
-